Pular para o conteúdo
Publicidade

Nascimento

Por Bíblia Online

O nascimento é obra das mãos de Deus. Cada criança é formada por Ele no ventre materno com propósito e amor. A Bíblia celebra a vida desde a concepção até a eternidade.

O nascimento de Jesus

O maior nascimento da história mudou o curso da humanidade. Jesus nasceu de uma virgem pelo poder do Espírito Santo, conforme as profecias.

Kubadwa kwa Yesu Khristu

Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.

Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, "Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo."

Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, "Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli," kutanthauza kuti, "Mulungu ali nafe."

Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.

Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli.

Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu

Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya.

Koma mngeloyo anati kwa iye, "Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha."

Mariya anafunsa mngeloyo kuti, "Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?"

Mngelo anayankha kuti, "Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu.

Formados desde o ventre

Deus nos teceu no ventre de nossa mãe. Antes de nascermos, Ele já nos conhecia e nos separou para um propósito sagrado.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;

munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;

ntchito zanu ndi zodabwitsa,

zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu

pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,

pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.

Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.

Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu

asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

"Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,

iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;

ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse."

Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.

Munachititsa kuti ndizikudalirani

ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.

Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;

kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.

Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;

Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,

ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.

"Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere

ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?

Ngakhale iye angathe kuyiwala,

Ine sindidzakuyiwala iwe!

Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,

koma osalola kuti abaledi mwana?" akutero Yehova.

"Kodi ndingatseke mimba

pa nthawi yoti abeleke?" akutero Mulungu wako.

Crianças — bênção e promessa

Jesus acolheu as crianças e disse: delas é o Reino dos céus. Os filhos são herança do Senhor e motivo de alegria para os pais.

Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."

Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba. Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.

Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha.

Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova;

Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.

Nascer de novo

Jesus ensinou que é preciso nascer de novo para ver o Reino de Deus. O novo nascimento é espiritual — pelo Espírito e pela Palavra.

Poyankha Yesu ananena kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu."

Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi.

Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.

Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;

nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.

Seja o primeiro