Nem só de pão vive o homem
'Nem só de pão vive o homem' — essa declaração de Jesus ao diabo no deserto revela que a Palavra de Deus é o verdadeiro alimento que sustenta a vida em plenitude.
O verdadeiro alimento
Quando tentado a transformar pedras em pão, Jesus respondeu com a Escritura: a vida humana depende de toda palavra que sai da boca de Deus.
Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ "
Mdierekezi anati kwa Iye, "Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza mwala uwu kuti usanduke buledi."
Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ "
Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.
Jesus, o pão vivo
Jesus é o pão da vida que desceu do céu. Quem come deste pão viverá para sempre. Ele é o sustento que satisfaz a fome da alma.
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, "Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.
Ine ndine chakudya chamoyo.
Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo."
Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse."
Buscar o Reino acima de tudo
Não andeis ansiosos pelo que comer ou beber. Buscai primeiro o Reino de Deus, e todas estas coisas vos serão acrescentadas.
Musade Nkhawa
"Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala?
Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.
Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, "Rabi idyani."
Koma Iye anawawuza kuti, "Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa."
Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, "Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?"
Yesu anati, "Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake.
Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa,
ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa.
Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso,
ndipo mʼminda musatuluke kanthu.
Ngakhale nkhosa
ndi ngʼombe zithe mʼkhola,
komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova,
ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.
Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga;
amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi,
amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo.