Publicidade

Ouvir

Por Bíblia Online

Ouvir é uma disciplina espiritual essencial. A Bíblia exorta: 'Quem tem ouvidos, ouça.' A fé vem pelo ouvir, e ouvir é mais que escutar — é obedecer e agir.

A fé vem pelo ouvir

Sem ouvir a Palavra, não há fé. A pregação do evangelho gera fé nos corações de quem ouve com disposição e humildade.

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?

Amene ali ndi makutu amve."

Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:

" Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.

Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.

Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,

mʼmakutu mwawo ndi mogontha,

ndipo atsinzina

kuti asaone kanthu.

Mwina angapenye ndi maso awo,

angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,

Ineyo nʼkuwachiritsa.

Ouvir e obedecer

Não basta ouvir — é preciso praticar. Quem ouve a Palavra e a pratica é como o homem sábio que edificou sobre a rocha.

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena.

Kumva ndi Kuchita

Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima.

Kumva ndi Kuchita

Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa

"Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe.

Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa

"Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu."

Yesu anayankha kuti, "Zalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ "

Koma Yesu anayankha kuti, "Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga."

Koma Yesu anayankha kuti, "Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga."

Muzichita chilichonse chimene mwaphunzira kapena kulandira kapena kumva kuchokera kwa ine kapena mwaona mwa ine. Ndipo Mulungu wamtendere adzakhala nanu.

Deus ouve nossas orações

O Senhor ouve os que clamam a Ele de coração sincero. Ele inclina os ouvidos para as nossas súplicas e responde com fidelidade.

Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;

Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.

Pakuti ananditchera khutu,

ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;

ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.

Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;

kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

Maso a Yehova ali pa olungama

ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;

Mmawa, Yehova mumamva mawu anga;

Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu

ndi kudikira mwachiyembekezo.

Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,

mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.

Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika,

pakuti ine ndimadalira Inu.

Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo,

pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.

Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera.

Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.

Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani.

Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.

Tchimo, Kuvomereza ndi Chipulumutso

Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa,

kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.

Ouvir a voz de Deus

Jesus disse: 'As minhas ovelhas ouvem a minha voz.' Deus fala através da Palavra, do Espírito e das circunstâncias — cabe a nós ouvir.

Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.

"Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.

Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.

Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.

Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.

Kodi Mulungu amene anakupatsani Mzimu wake ndi kuchita zodabwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumachita ntchito za lamulo kapena chifukwa mumakhulupirira zimene munamva?

Sabedoria no ouvir

Seja pronto para ouvir e tardio para falar. A sabedoria começa com a disposição de ouvir instrução e aceitar correção.

Ukayankha usanamvetse bwino nkhani,

umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.

Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino,

ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.

Chenjezo pa za Chigololo

Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;

ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.

Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,

koma wonyoza chidzudzulo amasochera.

Wokana kumvera malamulo

ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru

kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.

Zinthu zonse ndi zotopetsa,

kutopetsa kwake ndi kosaneneka.

Maso satopa ndi kuona

kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.

" Ngati mudzapitirira kutsutsana nane ndi kukana kundimvera, ndidzachulukitsa masautso anu kasanu ndi kawiri molingana ndi machimo anu.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, "Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu."

Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka."

"Nthawi ikubwera," Ambuye Yehova akunena kuti,

"Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;

osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,

koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.

Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera.

Yoswa anati kwa Aisraeli, "Bwerani pano mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu.

Chimene mwanena mu mdima chidzamveka dzuwa likuwala, ndipo zimene mwanongʼona mʼkhutu mʼchipinda chamʼkati, zidzayankhulidwa pa denga la nyumba.

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

"Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo.

Za Mʼbale Amene Akuchimwirani

"Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo. Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu. Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.

Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto.

"Mafunde a imfa anandizinga;

mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.

Anandimanga ndi zingwe za ku manda;

misampha ya imfa inalimbana nane.

"Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;

ndinapemphera kwa Mulungu wanga.

Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;

kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_12-11-46-