Publicidade

Gravidez e maternidade

Por Bíblia Online

Gravidez e maternidade são bênçãos celebradas na Bíblia. Deus forma cada criança no ventre, cuida da mãe e da família, e abençoa a geração dos justos.

Filhos são herança do Senhor

Deus abençoa a fertilidade e o crescimento das famílias. Cada criança é obra de suas mãos, conhecida e amada antes mesmo de nascer.

Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka.

Koma Aisraeli anaberekana ndi kuchuluka kwambiri nakhala amphamvu kwambiri, kotero kuti anadzaza dzikolo.

Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;

mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;

munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;

ntchito zanu ndi zodabwitsa,

zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu

pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,

pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.

Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.

Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu

asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,

ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,

koma osalola kuti abaledi mwana?" akutero Yehova.

"Kodi ndingatseke mimba

pa nthawi yoti abeleke?" akutero Mulungu wako.

Força e cuidado na gravidez

Deus dá forças à mulher grávida e a sustenta em cada etapa. Sua graça é suficiente e seu poder se aperfeiçoa na fraqueza.

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu.

Koma anandiwuza kuti, "Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka." Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Tcherani khutu lanu kwa ine,

bwerani msanga kudzandilanditsa;

mukhale thanthwe langa lothawirapo,

linga lolimba kundipulumutsa ine.

Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu

ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;

tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.

Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:

Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake

ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake

ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,

inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,

Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,

ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.

Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi

ndidzakusamalirani ndithu.

Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,

ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.

A bênção da maternidade

A Bíblia honra a maternidade como ministério sagrado. As mães são instrumentos de Deus para formar vidas e transmitir a fé.

Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

Ana ake amamunyadira ndipo amamutcha kuti wodala;

ndipo mwamuna wake, amamuyamikira nʼkumati,

Kaini ndi Abele

Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, "Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna."

Kubadwa kwa Isake

Yehova anakomera mtima Sara monga ananenera, ndipo Yehovayo anachita monga momwe analonjezera. Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza.

Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi.

Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, "Ndinachita kumupempha kwa Yehova."

Proteção divina

Deus protege a mãe e o bebê, guardando-os de todo mal. Ele acompanha cada momento com ternura e fidelidade.

Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba

adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

Ndidzanena za Yehova, "Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,

Mulungu wanga amene ndimadalira."

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;

adzasunga moyo wako.

Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;

kuyambira tsopano mpaka muyaya.

"Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,

iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;

ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse."

"Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza. Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo,

"Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere

ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?

Ngakhale iye angathe kuyiwala,

Ine sindidzakuyiwala iwe!

Esperança e promessa

A maternidade é caminho de esperança. Como Sara, Ana e Isabel, as mães encontram na fé a força para aguardar as promessas de Deus.

Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika.

Wodala iye amene wakhulupirira kuti chimene Ambuye wanena kwa iye chidzakwaniritsidwa!"

Nyimbo ya Mariya

Ndipo Mariya anati:

"Moyo wanga ulemekeza Ambuye.

Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

pakuti wakumbukira

kudzichepetsa kwa mtumiki wake.

Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,

pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,

dzina lake ndi loyera.

Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake

monga mayi wa ana wosangalala.

Tamandani Yehova.

Ndidzamudalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamudalitsa kuti akhale mayi wa mitundu ya anthu; mafumu a anthuwo adzachokera mwa iye."

Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka

mʼkati mwa nyumba yako;

ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi

kuzungulira tebulo lako.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-