Publicidade

Profecia

Por Bíblia Online

A profecia é a voz de Deus revelada ao seu povo. Através dos profetas, Deus comunicou seus planos, advertiu contra o pecado e anunciou a vinda do Messias.

Profecia e revelação divina

A profecia na Bíblia não é invenção humana, mas homens santos de Deus falaram movidos pelo Espírito Santo, revelando os mistérios divinos.

Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.

Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu

asanawulule zimene akufuna kuchita

kwa atumiki ake, aneneri.

Atamva zimenezi, anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera.

Profecias messiânicas cumpridas

As profecias do Antigo Testamento sobre o Messias se cumpriram em Jesus. Seu nascimento, ministério e sacrifício foram anunciados séculos antes.

Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli.

Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, "Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli," kutanthauza kuti, "Mulungu ali nafe."

Kubwera kwa Mfumu ya Ziyoni

Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!

Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu!

Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,

yolungama ndi yogonjetsa adani,

yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu,

pa mwana wamphongo wa bulu.

Kulungama Mwachikhulupiriro

Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni. Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina,

Discernimento profético

A Bíblia nos alerta para examinar tudo e reter o que é bom. Nem todo que profetiza fala da parte de Deus — devemos provar os espíritos.

Kuyesa Mizimu

Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.

Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.

Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.

Aneneri Owona ndi Onyenga

"Chenjerani nawo aneneri onyenga. Amabwera kwa inu atavala zikopa zankhosa, koma mʼkati mwawo ali mimbulu yolusa.

Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.

Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu.

Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu. Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi a aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pa ngodya.

"Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova.

Seja o primeiro
Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-