Pular para o conteúdo
Publicidade

Reino

Por Bíblia Online

O Reino de Deus é o tema central da pregação de Jesus. Desde o início de seu ministério, Ele proclamou: 'Arrependei-vos, porque é chegado o Reino dos céus.'

O anúncio do Reino

Jesus inaugurou seu ministério proclamando a chegada do Reino. Ele convida todos ao arrependimento e à fé nessa nova realidade.

Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, "Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira."

"Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!"

Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, Ufumu wa Mulungu wayandikira.

Ngokongoladi mapazi a

amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri.

Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere,

chisangalalo ndi chipulumutso.

Iwo akubwera kudzawuza anthu

a ku Ziyoni kuti,

"Mulungu wako ndi mfumu!"

A natureza do Reino

O Reino de Deus é governo soberano do Senhor sobre todas as coisas. Ele é o Rei eterno, imortal e invisível.

Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu,

ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola.

Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu.

Wanu, Inu Yehova ndi ufumu;

Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?

Yehova Wamphamvuzonse,

Iye ndiye Mfumu yaulemerero.

Sela

Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,

Yehova ndiye wotilamulira,

Yehova ndiye mfumu yathu;

ndipo ndiye amene adzatipulumutse.

Ndipo Yehova adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo padzakhala Ambuye mmodzi yekha, ndipo dzina lidzakhala limodzi lomwelo.

Entrar no Reino

Para entrar no Reino é preciso nascer de novo, tornar-se como criança e buscar primeiro a justiça de Deus acima de tudo.

Poyankha Yesu ananena kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu."

Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.

Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.

Yesu anati, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa."

Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,

pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo."

Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba."

Cidadãos do Reino

Os cristãos são concidadãos dos santos e membros da família de Deus, chamados a viver dignamente do Reino que receberam.

Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu. Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi a aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pa ngodya.

Chuma cha Kumwamba

"Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu.

Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.

Seja o primeiro