Publicidade

Ezequiel 19

Nyimbo ya Maliro a Akalonga a Israeli

1 "Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli. 2 Uzinena kuti,

" ‘Amayi ako anali ndani?

Anali ngati mkango waukazi!

Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna;

unkalera ana ake pakati pa misona.

3 Unalera mmodzi mwa ana ake,

ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu.

Unaphunzira kugwira nyama,

ndipo unayamba kudya anthu.

4 Anthu amitundu anamva za mkangowo,

ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo.

Iwo anawukoka ndi ngowe

kupita nawo ku dziko la Igupto.

5 " ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera,

amayiwo anatenganso mwana wina

namusandutsa mkango wamphamvu.

6 Unkayendayenda pakati pa mikango inzake,

pakuti tsopano unali mkango wamphamvu.

Unaphunzira kugwira nyama

ndipo unayamba kudya anthu.

7 Unagwetsa malinga awo,

ndikuwononga mizinda yawo.

Onse a mʼdzikomo

anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.

8 Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira,

inabwera kudzalimbana nawo.

Anawutchera ukonde wawo,

ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.

9 Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga.

Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni

ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende

ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso

ku mapiri a Israeli.

10 " ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa

wodzalidwa mʼmbali mwa madzi.

Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri

chifukwa cha kuchuluka kwa madzi.

11 Nthambi zake zinali zolimba,

zoyenera kupangira ndodo yaufumu.

Unatalika nusomphoka pakati pa

zomera zina.

Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake,

ndi nthambi zake zambiri.

12 Koma unazulidwa mwaukali

ndipo unagwetsedwa pansi.

Unawuma ndi mphepo ya kummawa,

zipatso zake zinayoyoka;

nthambi zake zolimba zinafota

ndipo moto unapsereza mtengo wonse.

13 Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu,

dziko lowuma ndi lopanda madzi.

14 Moto unatulukanso mu mtengomo

ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake.

Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo

yoyenera kupangira ndodo yaufumu.

Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ "

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_10-32-54-