Seguir a Jesus
Seguir a Jesus é o convite mais transformador da Bíblia. Jesus chamou pescadores, cobradores de impostos e pessoas comuns para deixar tudo e segui-lo. Esse chamado continua vivo hoje.
O chamado de Jesus
Jesus disse: 'Segue-me'. Esse convite simples e poderoso mudou a vida de pescadores, publicanos e pessoas comuns ao longo da história.
Yesu anati, "Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu." Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
Kuyitanidwa kwa Mateyu
Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye, "Nditsate Ine." Ndipo iye ananyamuka namutsata.
Yesu Ayitana Filipo ndi Natanieli
Pa tsiku lotsatira Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Atamupeza Filipo, anati kwa iye, "Nditsate."
Kutsatira Yesu
Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, "Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita."
Yesu anayankha kuti, "Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake."
Iye anati kwa wina, "Nditsate Ine."
Koma munthuyo anayankha kuti, "Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga."
Yesu anati kwa iye, "Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu."
Koma winanso anati, "Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa."
Yesu anayankha kuti, "Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu."
O custo do discipulado
Seguir a Jesus exige renúncia. É preciso tomar a cruz diariamente, deixar tudo para trás e amar a Cristo acima de qualquer outro vínculo.
Za Kusenza Mtanda
Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine.
"Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.
Petro anati kwa Iye, "Ife tasiya zonse ndi kukutsatani!"
Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo. Koma ambiri amene ndi woyambirira adzakhala omalizira, ndipo omalizira adzakhala oyambirira."
Caminhar com Cristo
Quem segue a Jesus não anda em trevas, mas tem a luz da vida. Ele nos convida a crescer nele e a servir como Ele serviu.
Za Umboni wa Yesu
Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, "Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo."
Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.
Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.
"Iye sanachite tchimo
kapena kunena bodza."
Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama.
Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo.
Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.