Temor dos homens
O temor dos homens é uma armadilha que paralisa a fé. A Bíblia nos convida a trocar o medo humano pela confiança em Deus, que é nosso refúgio e escudo.
Não temas os homens
Deus é a nossa luz e salvação — de quem teremos medo? A Escritura nos encoraja a não temer aqueles que podem destruir o corpo, mas não a alma.
Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane
kudzadya mnofu wanga,
pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,
iwo adzapunthwa ndi kugwa.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,
mtima wanga sudzaopa.
Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,
ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.
Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.
"Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.
Confiança em Deus acima do medo
Quando tememos a Deus, o medo dos homens perde o poder. O Senhor está conosco, e se Ele é por nós, quem será contra nós?
Ndikachita mantha
ndimadalira Inu.
Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda,
mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha.
Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?
Yehova ali nane; sindidzachita mantha.
Munthu angandichite chiyani?
Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,
"Ambuye ndiye mthandizi wanga;
sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?"
Musawaope chifukwa Yehova Mulungu mwini adzakumenyerani nkhondo."
Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu.