Publicidade

Vida nova

Por Bíblia Online

Em Cristo, toda pessoa é transformada em uma nova criação. O velho passa e tudo se faz novo. A vida nova é o resultado da obra redentora de Jesus em nosso coração.

Morte e ressurreição com Cristo

O batismo simboliza nossa morte para o pecado e ressurreição para uma nova vida. Fomos sepultados com Cristo e ressuscitamos com Ele.

Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.

Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake. Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.

Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.

Nova criação

Quando aceitamos Jesus, nascemos de novo. A velha natureza dá lugar a uma identidade renovada pelo Espírito Santo.

Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.

Despir o velho, vestir o novo

A vida nova se manifesta em abandonar os velhos hábitos e revestir-se do novo homem, criado segundo a vontade de Deus.

Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero.

Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa. Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Renovação interior

Deus promete dar um coração novo e um espírito novo. A transformação nasce do arrependimento e da purificação divina.

Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu

ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.

Musandichotse pamaso panu

kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.

Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu

ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga.

Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse. Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.

Seja o primeiro
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-07-05_12-11-46-