Publicidade

1 Pedro 1

6 Zimenezi zikukondweretseni kwambiri, ngakhale tsopano, kwa kanthawi kochepa, mukumva zowawa mʼmayesero osiyanasiyana. 7 Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. 8 Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. 9 Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-