10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, "Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye."
11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha.