Pular para o conteúdo
Publicidade

CHIVUMBULUTSO 7

Anthu 144,000

1 Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse. 2 Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti, 3 "Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu." 4 Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.

5 Ochokera fuko la Yuda analipo 12,000 amene analembedwa chizindikiro.

Ochokera fuko la Rubeni analipo 12,000;

ochokera fuko la Gadi analipo 12,000;

6 ochokera fuko la Aseri analipo 12,000;

ochokera fuko la Nafutali analipo 12,000;

ochokera fuko la Manase analipo 12,000;

7 ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000;

ochokera fuko la Levi analipo 12,000;

ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;

8 ochokera fuko la Zebuloni analipo 12,000;

ochokera fuko la Yosefe analipo 12,000;

ochokera fuko la Benjamini analipo 12,000.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também