36 Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, "Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?" 37 Filipo anati, "Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa." Ndunayo inayankha kuti, "Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu." 38 Ndipo analamulira galeta kuti liyime. Onse awiriwo, Filipo ndi Ndunayo anatsika ndi kulowa mʼmadzi ndipo Filipo anamubatiza.
Publicidade
Publicidade