6 Nʼchimodzimodzinso Abrahamu, "Iye anakhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu anamutenga kukhala wolungama."
7 Tsono zindikirani kuti amene akhulupirira, ndi ana a Abrahamu. 8 Malemba anaonetseratu kuti Mulungu adzalungamitsa anthu a mitundu ina mwachikhulupiriro, ndipo ananeneratu Uthenga Wabwino kwa Abrahamu kuti, "Mitundu yonse ya anthu idzadalitsika kudzera mwa iwe." 9 Choncho iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndi odalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu, munthu wachikhulupiriro.