Pular para o conteúdo
Publicidade

GENESIS 2

18 Ndipo Yehova Mulungu anati, "Sibwino kuti munthu akhale yekha. Ndidzamupangira mnzake womuthandiza."

19 Kenaka Yehova Mulungu anawumba ndi dothi nyama zonse zakuthengo ndi mbalame zonse zamlengalenga. Ndipo Iye anapita nazo kwa munthu uja kuti akazipatse mayina; ndipo dzina lililonse limene Adamu anapereka ku chamoyo chilichonse, lomwelo linakhala dzina lake. 20 Choncho Adamu anazitcha mayina ziweto zonse, mbalame zamlengalenga ndi nyama zakuthengo zonse.

Komabe munthu uja analibe mnzake womuthandiza. 21 Tsono Yehova Mulungu anamugonetsa munthu uja tulo tofa nato; ali mtulo chomwecho, Mulungu anachotsa imodzi mwa nthiti zake ndi kutseka pamalopo ndi mnofu. 22 Motero Yehova Mulungu anapanga mkazi ndi nthiti ija imene anatenga kwa munthu uja nabwera naye kwa iye.

23 Munthu uja anati,

"Uyu ndiye fupa lochokera ku mafupa anga

ndi mnofu wochokera ku mnofu wanga;

adzatchedwa mkazi,

popeza wachokera mwa mwamuna."

24 Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.

Veja também