7 Kenaka Yosefe anapita ndi abambo ake kwa Farao kukawaonetsa, ndipo Yakobo anadalitsa Faraoyo. 8 Atatero, Farao anafunsa Yakobo kuti, "Muli ndi zaka zingati?"
9 Yakobo anayankha kuti, "Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka za moyo wanga ndi zowerengeka, komanso zakhala zaka za masautso. Zaka za moyo wanga sizingafanane ndi zaka za moyo wa makolo anga." 10 Atatha kumudalitsa Farao uja, Yakobo anatsanzika nʼkunyamuka.
11 Choncho Yosefe anakhazika abambo ake aja ndi abale ake mʼdziko la Igupto. Iye anawapatsa dera la Ramesesi limene linali dziko lachonde kwambiri monga analamulira Farao. 12 Yosefe anaperekanso chakudya kwa abambo ake, kwa abale ake ndi kwa onse a mʼnyumba ya abambo ake monga mwa chiwerengero cha ana awo.