5 Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. 6 Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.
Publicidade