Pular para o conteúdo
Publicidade

YOBU 38

4 "Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?

Ndiwuze ngati ukudziwa.

5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!

Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?

6 Kodi maziko ake anawakumba potani,

kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,

7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi

ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?

8 "Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,

pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,

9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake

ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,

10 pamene ndinayilembera malire ake

ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.

11 Pamene ndinati, Ufike mpaka apa ndipo usapitirire

apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também