Publicidade

Jó 25

Mawu a Bilidadi

1 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

2 "Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,

Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.

3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?

Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?

4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?

Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?

5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,

ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,

6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,

mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!"

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-19_11-20-24-