5 Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga,
koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga.
6 Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi,
ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa."
Mulungu Adalitsa Yobu
7 Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, "Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu.