Pular para o conteúdo
Publicidade

João 14

21 Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye."

22 Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, "Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?"

23 Yesu anamuyankha kuti, "Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24 Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

Veja também