13 Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. 14 Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. 15 Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. 16 Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, "Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!"
17 Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, "Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa."