Yesu Aonekera kwa Ophunzira ake Tomasi Palibe
19 Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, "Mtendere ukhale nanu!" 20 Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye.
21 Yesu anatinso, "Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani." 22 Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, "Landirani Mzimu Woyera. 23 Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe."