Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya
1 Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: 2 Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. 3 Simoni Petro anawawuza iwo kuti, "Ine ndikupita kukasodza," ndipo iwo anati, "ife tipita nawe." Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
4 Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.
5 Yesu anawafunsa iwo kuti, "Anzanga, kodi muli nsomba?"
Iwo anayankha kuti, "Ayi."
6 Iye anati, "Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu." Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.
7 Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, "Ndi Ambuye!" Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. 8 Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. 9 Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.
10 Yesu anawawuza kuti, "Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo."
11 Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike.