4 Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, 5 "Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. 6 Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. 7 Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino."
Publicidade