1 Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa.
2 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, "Taona ndapereka Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake mʼmanja mwako. 3 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse muzizungulira mzindawu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku. 4 Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga. 5 Ansembe adzalize malipenga kosalekeza. Tsono anthu onse akadzamva kuliza kumeneku adzafuwule kwambiri, ndipo makoma a mzindawo adzagwa. Zikadzatero ankhondo adzalowe mu mzindawo."
6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anayitana ansembe ndipo anawawuza kuti, "Nyamulani Bokosi la Chipangano cha Yehova ndipo ansembe asanu ndi awiri anyamule malipenga. Iwowa akhale patsogolo pake." 7 Ndipo analamulira anthu kuti, "Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova."