4 "Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
Ndiwuze ngati ukudziwa.
5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
6 Kodi maziko ake anawakumba potani,
kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
8 "Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
9 pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
10 pamene ndinayilembera malire ake
ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
11 Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’