Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 18

Yesu Achiritsa Wosaona

35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. 37 Iwo anamuwuza kuti "Yesu wa ku Nazareti akudutsa."

38 Iye anayitana mofuwula, "Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!"

39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, "Mwana wa Davide, chitireni chifundo!"

40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, 41 "Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?"

Iye anayankha kuti, "Ambuye, ine ndifuna ndionenso."

42 Yesu anati kwa iye, "Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa." 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.

Veja também