43 Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. 44 Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.
45 Yesu anafunsa kuti, "Wandikhudza ndani?"
Onse atakana, Petro anati, "Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani."
46 Koma Yesu anati, "Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine."
47 Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. 48 Kenaka anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere."