49 Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, "Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa."
50 Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, "Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa."
51 Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. 52 Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, "Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo."
53 Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. 54 Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, "Mwana wanga, dzuka!" 55 Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. 56 Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.