Yesu Adalitsa Ana
13 Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula. 14 Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, "Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa. 15 Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo." 16 Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.