Pempho la Mkazi wa Zebedayo
20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.
21 Yesu anawafunsa kuti, "Mukufuna chiyani?"
Amayiwo anati, "Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu."
22 Yesu anawawuza kuti, "Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?"
Iwo anayankha nati, "Inde tingathe."
23 Yesu anawawuza kuti, "Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga."