Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 21

Yesu Alowa mu Yerusalemu

1 Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2 nawawuza kuti, "Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine. 3 Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo."

4 Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri:

5 "Uza mwana wamkazi wa Ziyoni,

taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,

yofatsa ndi yokwera pa bulu,

pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu."

6 Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira. 7 Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo. 8 Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo. 9 Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti,

"Hosana Mwana wa Davide!"

"Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!"

"Hosana mmwambamwamba!"

10 Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, "Ndani ameneyu?"

11 Magulu a anthu anayankha kuti, "Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti."

Veja também