1 "Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. 2 Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. 3 Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; 4 koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. 5 Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona.
6 "Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’
7 "Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo. 8 Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’
9 "Ochenjerawo anayankha, nati, ‘Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.’
10 "Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa.
11 "Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’
12 "Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’
13 "Choncho khalani odikira, popeza simudziwa tsiku kapena nthawi."