Pular para o conteúdo
Publicidade

Mateus 5

3 "Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,

chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

4 Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

5 Odala ndi amene ali ofatsa,

chifukwa adzalandira dziko lapansi.

6 Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,

chifukwa adzakhutitsidwa.

7 Odala ndi amene ali ndi chifundo,

chifukwa adzawachitira chifundo.

8 Odala ndi amene ali oyera mtima,

chifukwa adzaona Mulungu.

9 Ndi odala amene amabweretsa mtendere,

chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

10 Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,

pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo."

11 "Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. 12 Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Veja também