Chikhulupiriro cha Kenturiyo
5 Yesu atalowa mʼKaperenamu, Kenturiyo anabwera kwa Iye napempha chithandizo, 6 nati, "Ambuye, wantchito wanga ali chigonere ku nyumba, sakuthanso kuyenda, akumva kuwawa kwambiri."
7 Ndipo Yesu anati kwa iye, "Ine ndibwera kudzamuchiritsa."
8 Kenturiyo uja anayankha kuti, "Ambuye, ndine wosayenera kuti Inu mukalowe mʼnyumba mwanga. Koma mungonena mawu ndipo wantchito wanga adzachiritsidwa. 9 Pakuti inenso ndili pansi pa ulamuliro ndipo ndili ndi asilikali amene ndiwalamulira. Ndikalamulira mmodzi kuti, ‘Pita,’ amapita; ndi kwa wina kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikawuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ iye amachita."
10 Yesu atamva zimenezi, anadabwa ndipo anati kwa omutsatira, "Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti sindinapeze wina aliyense mu Israeli wachikhulupiriro chachikulu chotere. 11 Ndikuwuzani kuti ambiri adzabwera kuchokera kummawa ndi kumadzulo, nadzakhala nawo pa phwando pamodzi ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba. 12 Koma eni ake ufumuwo adzaponyedwa ku mdima wakunja kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano."
13 Pamenepo Yesu anati kwa Kenturiyo, "Pita! Zichitike monga momwe wakhulupirira." Ndipo wantchito wake anachira pa nthawi yomweyo.