17 Ndinawawuza kuti, "Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi." 18 Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza.
Tsono anati, "Tiyeni tiyambenso kumanga." Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.