Pular para o conteúdo
Publicidade

NEHEMIYA 7

1 Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. 2 Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. 3 Ine ndinawawuza kuti, "Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo."

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

4 Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. 5 Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

6 Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. 7 Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

8 Zidzukulu za Parosi 2,172

   9 Zidzukulu za Sefatiya 372

   10 Zidzukulu za Ara 652

   11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu) 2,818

   12 Zidzukulu za Elamu 1,254

   13 Zidzukulu za Zatu 845

   14 Zidzukulu za Zakai 760

   15 Zidzukulu za Binuyi 648

   16 Zidzukulu za Bebai 628

   17 Zidzukulu za Azigadi 2,322

   18 Zidzukulu za Adonikamu 667

   19 Zidzukulu za Abigivai 2,067

   20 Zidzukulu za Adini 655

   21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya) 98

   22 Zidzukulu za Hasumu 328

   23 Zidzukulu za Bezayi 324

   24 Zidzukulu za Harifu 112

   25 Zidzukulu za Gibiyoni 95.

   26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa 188

   27 Anthu a ku Anatoti 128

   28 Anthu a ku Beti-Azimaveti 42

   29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti 743

   30 Anthu a ku Rama ndi Geba 621

   31 Anthu a ku Mikimasi 122

   32 Anthu a ku Beteli ndi Ai 123

   33 Anthu a ku Nebo winayo 52

   34 Ana a Elamu wina 1,254

   35 Zidzukulu za Harimu 320

   36 Zidzukulu za Yeriko 345

   37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono 721

   38 Zidzukulu za Senaya 3,930.

39 Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa) 973

40 Zidzukulu za Imeri 1,052

41 Zidzukulu za Pasi-Huri 1,247

42 Zidzukulu za Harimu 1,017.

43 Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya 74.

44 Anthu oyimba:

   Zidzukulu za Asafu 148.

45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za

   Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai 138.

46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za

   Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,

   47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni

   48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,

   49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,

   50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,

   51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,

   52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,

   53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,

   54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,

   55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema

   56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

57 Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za

   Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida

   58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,

   59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu

   zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.

60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo 392.

61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

62 Zidzukulu za

   Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda 642.

63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za

Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também