4 Apo mfumu inandifunsa kuti, "Tsono ukufuna kundipempha chiyani?"
Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. 5 Ndipo ndinayankha kuti, "Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso."