Adani a Nehemiya pa Ntchito Yake
1 Sanibalati atamva kuti tikumanganso khoma anapsa mtima nayamba kuseka ndi kunyogodola Ayuda kwambiri. 2 Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, "Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?"
3 Tobiya wa ku Amoni, amene anali naye anati, "Chimene akumangacho ngati nkhandwe itakwerapo, itha kugwetsa khoma lawolo!"