Kulemekeza Mulungu
33 Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri!
Ndani angazindikire maweruzidwe ake,
ndipo njira zake angazitulukire ndani?
34 "Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye?
Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?"
35 "Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu,
kuti Mulunguyo amubwezere iye?"
36 Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye.
Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.