16 Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti,
"Usaope, iwe Ziyoni;
usafowoke.
17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako,
ali ndi mphamvu yopulumutsa.
Adzakondwera kwambiri mwa iwe,
adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake,
adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe."