Pular para o conteúdo
Publicidade

Agradecimento pela vida

Por Bíblia Online

Agradecer pela vida é reconhecer que cada respiração é dom de Deus. Toda criatura que tem fôlego louve ao Senhor — porque Ele nos formou e nos sustenta com amor.

Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.

Tamandani Yehova.

Tamandani Yehova.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;

ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;

munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.

Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;

ntchito zanu ndi zodabwitsa,

zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu

pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,

pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.

Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.

Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu

asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;

ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.

Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,

pamene ndikusangalala mwa Yehova.

Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.

Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;

ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko

ndi ku mabwalo ake ndi matamando;

muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.

Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!

Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu

amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.

Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;

Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.

Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;

mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

Ndidzakukwezani Yehova,

chifukwa mwanditulutsa kwakuya,

ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.

Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo

ndipo Inu munandichiritsa.

Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,

munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse;

ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.

Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu;

Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.

Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Madalitso Auzimu mwa Khristu

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.

Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!

ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika. Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.

Kupambana Koposa kwa Khristu

Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye.

Mukadya ndi kukhuta, yamikani Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.

Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga;

munapulumutsa moyo wanga.

Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri;

mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha.

Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo,

Inu Yehova Mulungu wanga.

"Pamene moyo wanga umachoka mwa ine,

ine ndinakumbukira Inu Yehova,

ndipo pemphero langa linafika kwa inu,

ku Nyumba yanu yopatulika.

Seja o primeiro