15 Farao anati kwa Yosefe, "Ndinalota maloto ndipo palibe amene watha kunditanthauzira. Tsono ndawuzidwa kuti iwe ukamva loto umadziwanso kulimasulira."
16 Yosefe anamuyankha Farao kuti, "Sindingathe koma Mulungu apereka yankho limene Farao akufuna."