10 Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale. 11 Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12 Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000. 13 Anaberekanso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu. 14 Mwana wake wamkazi woyamba anamutcha Yemima, wachiwiri anamutcha Keziya, wachitatu anamutcha Kereni Hapuki. 15 Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.
16 Zitachitika zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140. Iye anaona zidzukulu zake mpaka mʼbado wachinayi. 17 Potsiriza, Yobu anamwalira ali nkhalamba ya zaka zochuluka kwambiri.