Pular para o conteúdo
Publicidade

João 11

Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro

1 Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. 2 Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. 3 Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, "Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala."

4 Atamva izi, Yesu anati, "Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo." 5 Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. 6 Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.

7 Kenaka anati kwa ophunzira ake, "Tiyeni tibwerere ku Yudeya."

8 Ophunzira akewo anati, "Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?"

9 Yesu anayankha kuti, "Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. 10 Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe."

11 Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, "Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa."

12 Ophunzira ake anayankha kuti, "Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino." 13 Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.

14 Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, "Lazaro wamwalira.

Veja também