Ku Nyumba ya Wowumba Mbiya
1 Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2 "Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga." 3 Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. 4 Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
5 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, 6 "Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?" akutero Yehova. "Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.