Publicidade

Jeremias 29

11 Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani," akutero Yehova, "ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. 12 Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. 13 Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse 14 mudzandipezadi," akutero Yehova, "ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali," akutero Yehova, "ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-