31 "Masiku akubwera," akutero Yehova,
"pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
ndiponso nyumba ya Yuda.
32 Silidzakhala ngati pangano
limene ndinachita ndi makolo awo
pamene ndinawagwira padzanja
nʼkuwatulutsa ku Igupto;
chifukwa anaphwanya pangano langa,
ngakhale ndinali mwamuna wawo,"
akutero Yehova.
33 "Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
atapita masiku amenewo," akutero Yehova.
"Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo
ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo
ndipo iwo adzakhala anthu anga.